Mavuto okhudza misonkho omwe anthu ochita bizinezi ya ma minibus amakumana nawo ati akuyembekezeka kuchepa kamba koti bungwe lotolera misonkho mdziko muno la Malawi Revenue Authority (MRA) lati likonza ena mwa mavutowa.
Wapampando wa bungwe la eni minibus la Minibus Owners Association of Malawi MOAM a Christopher Chisesere ndiwo anena izi pambuyo pa msonkhano womwe mabungwe awiriwa anali nawo mu mzinda wa Blantyre.
Iwo ati bungwe lawo ndi lokondwa kamba koti bungwe lotolera misonkholi latsimikiza kuti lichitapo kanthu pothana ndi vuto la misonkho lomwe akukumana nalo.
A Chisesere ati bungweli silimamvetsa cholinga cha msonkho womwe eni ma minibuswa amayenera kupereka pa miyezi itatu iliyonse, ndipo ati kuyambira pano liwonetsetsa kuti lizipereka msonkho munthawi yake kamba ka mmene bungwe la MRA lafotokozera.
Pa msonkhanowo bungwe la MOAM lapempha boma kuti liwaganizire powonjezera zaka za galimoto zomwe zikuyenera kuloledwa kulowa mdziko muno osalipira msonkho, kuti zikhale zaka zisanu ndi zitatu.
Msonkhanowo cholinga chake chinali kudziwitsa eni minibus za kusintha kwa malamulo ena makamaka okhudza misonkho yatsopano yomwe boma linakhazikitsa.