Quantcast
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dziko la Gambia Ndi Lokonzeka Kuthetsa Mgwirizano Ndi Bungwe la EU

Dziko la Gambia lati ndilokonzeka kuthetsa mgwilizano wake ndi bungwe la European Union (EU) ngati bungweli lipitilize kukakamiza dzikolo, kuvomeleza kuti anthu azichita maukwati apakati pa amuna kapena akazi okhaokha.

Nduna yowona nkhani za kunja kwa dzikolo a Bala Garba Jahumpa, ati mtsogolei wa dzikolo Yahya Jammeh wanenetsa kuti sangalore kuti m’chitidwe wa maukwati achilendowa uzichitika m’dzikomo, kamba koti pachikhalidwe cha dzikolo sizololedwa.

Iye wadzudzulanso mabungwe omwe akumabwera m’dzikomo ndi zolinga zodzapeleka thandizo ngati njira imodzi yokopera dzikolo kuti livomeleze za maukwati osavomelezekawa.

Dziko la Gambia ndi limodzi mwa mayiko a mu Africa amene anasayinilana pangano loti onse opezeka akuchita maukwati achilendowa aziyimbidwa mlandu ndipo akapezeka olakwa azikakhala kundende moyo wawo wonse.

Padakali pano dziko la Gambia lati limemeza mayiko ena amu Africa kuti asavomeleze zoti mayiko a azungu abwere ndi zikhalidwe zoyipa mmayiko a Africa.

Dziko la Uganda nalo likuyembekezeka kuchitanso kawuniwuni wa malamulo okhudza mchitidwe wa maukwati apakati pa amuna kapena akazi okhaokhawa amene samavomelezedwanso mdzikomo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>