Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Achitepo Kanthu Polimbana ndi Matenda a Edzi

$
0
0

Tsiku lokumbukira matenda a Edzi padziko lonse ati likuyenera kukhala tsiku limene anthu akuyenera kukumbukira kuti matenda a Edzi alipodi, pochitapo kanthu polimbana ndi matendawa. 

Wachiwiri kwa mkulu woyang’anira mapulogalamu ku Radio Maria Malawi Bambo Charles Kaponya ndi omwe anena izi lolemba pamwambo okumbukira matenda a Edzi womwe unachitika mdera la Mpinganjira m’boma la Mangochi pamene dziko lonse limakumbukira za matendawa pa tsikuli.

Bambo Kaponya ati patsikuli anthu akuyenera kudziwa kuti Edzi ilipodi ndipo akuyenera kutsatira njira zopewera kuti pasakhale anthu atsopano otenga matenda,pasakhale kusala anthu ali ndi matendawa komanso pasakhale imfa zodza chifukwa cha matendawa.

“Tsiku ngati limeneli ndi lofunika kwambiri kamba koti anthu akuyenera kukhala pansi mmabanja mwawo ndi malo osiyanasiyana amene anthu amasonkhana ndi kupeza njira zogonjetsera mliriwu,” anatero Bambo Kaponya.

Iwo ati aliyense ali ndi udindo wotengapo gawo kupeza njira zothandiza kuti kachilombo koyambitsa matendawa kasapitilire kufala.

Polankhulapo mmodzi mwa anthu omwe anapezeka ndi matendawa Mayi Bibiyana Yadi ati anthu azikhala omasuka kukayezetsa komanso kulandira thandizo akapezeka ndi matendawa.

Iwo alimbikitsa anthu omwe anapezeka ndi matendawa kuti asabwelere mmbuyo mu ntchito zawo. 

Pakadali pano dziko la Malawi lati likufuna kuti anthu 90 pa 100 aliwonse asatengenso matendawa,asamasale anzawo komanso pasakhale imfa zina.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>