Mabungwe omenyelera ufulu wa achinyamata mdziko muno apereka masiku khumi ndi anayi 14, kuti mabungwe omwe analandira ndalama kuthumba la bungwe lowona za matenda a Edzi la National Aids Commission NAC, akhale atabweza ndalamazi.
Mabungwewa omwe ndi oposa anayi alankhula izi kudzera mu chikalata chomwe atulutsa pa 1 December 2014, ngati njira imodzi yoganizira matenda a Edzi.
Iwo ati akugwirizana ndi mabungwe a CHRR, MEHEN, MANERERA+, CEDEP ndi MANET+, omwenso anasonyeza kukhudzidwa ndi nkhaniyi, ndipo apempha mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika, kuti achotse mmaudindo akuluakulu onse a bungweli.
Iwo ati ndiwokhudzidwa powona ndalama zokwana 57 million, 4 hundred thousand kwacha zikuperekedwa ku mabungwe a Mulhako wa Alhomwe, Nthambi ya Boma ya Ukazitape ndi bungwe la mkazi wamtsogoleri wadziko lino la BEAM Trust.
Malinga ndi chikalatacho mabungwewa salekelera kuti boma liziwononga ndalama pa zinthu zosayenera, pamene achinyamata akuvutika mu njira zosiyanasiyana monga umphawi komanso matenda a Edzi.
Mabungwewa apempha bungwe la NAC kuti lifotokozere amalawi momveka bwino chomwe chidachitika kuti ndalamazi zipite mmabungwe atatuwa omwe sagwira ntchito zokhudza matenda a Edzi mdziko muno.