Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo wa Katolika Susintha Chiphunzitso Chake pa Banja

$
0
0

Episkopi wa Arkidayosizi ya Sydney mdziko la Australia Ambuye Anthony Fisher, atsimikizira a khristu a mpingo wakatolika mdzikolo kuti anthu asayembekezere kuti mpingowu, usintha chiphunzitso chake pankhani yokhudza banja.

Ambuye Fisher omwe angosankhidwa kumene paudindowu anena izi pothilirapo ndemanga pakawuniwuni yemwe mpingowu ukuchita pankhani yokhudza banja.

Iwo anena izi pamene mpingowu ukukonzekeranso msonkhano wachiwiri wa maepiskopi wokambirana ena mwa malamulo a mpingowu pankhani yokhudza banja womwe udzachitikire kulikulu la mpingowu ku Vatican mmwezi wa November chaka cha mawa.

Ambuye Fisher ati pokhazikitsa kawuniwuniyu, cholinga cha mtsogoleri wampingowu padziko lonse Papa Francisco, ndi chofuna kufikira anthu onse ndi uthenga wabwino popanda zopinga zilizonse mmabanja awo.

 

 

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>