Bungwe lomenyera ufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi CAMA, layamba layimitsa ziwonetsero zomwe linakonza kuti zichitike lachinayi pokwiya ndi vuto la madzi lomwe lafika poyipa kwambiri mu mzinda wa Blantyre.
Mkulu wabungweli a John Kapito ndi yemwe wanena izi pambuyo pa mkumano womwe bungwe la Blantyre Water Board linakonzera bungwe la CAMA, pofuna kutsimikizira bungweli kuti likonza mavuto omwe likudandaula.
A Kapito awuza Radio Maria Malawi kuti bungwe la Blantyre Water Board, lalonjeza kuti liyamba kupereka madzi mmadera onse omwe sakulandira madzi pogwiritsa ntchito galimoto zonyamula madzi, ndipo lizidziwitsa anthu tsiku ndi tsiku mmadera awo za malo omwe galimotozo ziziyima kudzera pawayilesi komanso nyuzipepala, kufikira pomwe vutoli lidzathe.
Iwo ati bungwe la CAMA likhala likuwonetsetsa kwa sabata imodzi kapena ziwiri kuti zomwe bungwe la Blantyre Water Board lalonjeza zikukwaniritsidwa.
“A Blanytre Water Board avomera kupanga zomwe ife tikufuna, tawapatsa mwayi kuti tiwone ngati akwaniritse zomwe alonjezazo,” anatero a Kapito.
Pothirirapo ndemanga, wapampando wa bungwe la Blantyre Water Board a James Naphambo, wati vuto la madzi mumzindawo lafika poyipa chifukwa cha ntchito zikuluzikulu zomwe bungweli likugwira.
Iwo ati ayesetsa kupereka madzi moyembekezera mmadera omwe akhudzidwa kwambiri ndi vutoli kufikira pomwe vutoli lidzathe.
“Amalawi ayembekezere kuti pofika miyezi ya February ndi March chaka chikudzachi vuto la madzi likhala litatha,” anatero a Naphambo.
Padakali pano bungweli lati liyesetsa kupeza njira kuti anthu mmadera osiyanasiyana amene akuvutika ndi vutoli, akhale ndi madzi.