Mabungwe Manet+, Manerela+,Cedep,Mehen komanso CHRR,alangiza mabungwe omwe adalandira ndalama kubungwe la NAC mosavomerezeka kuti abweze ndalamazi pasanathe sabata imodzi.
Mabungwewa anena izi lachitatu pamsonkhano wa atolankhani omwe anachititsa mu mzinda wa Lilongwe.
Iwo anena izi pambuyo pamsonkhano wina womwe anachititsa posachedwapa mu mzindawo pomwe amapempha akuluakulu a kubungwe la NAC kuti atule pansi maudindo awo chifukwa cholephera ntchito yawo.
Mabungwewa apereka sabata imodzi kuti pempho lawo limveke ndipo ati ngati sizitheka, amemeza anthu kuti achite ziwonetsero pokwiya ndi nkhaniyi.
Posachedwapa mkazi wa mtsogoleri wa dziko lino Mai Getrude Mutharika yemwe bungwe lake ndi limodzi mwa mabungwe omwe adalandira ndalamazi, anawuza amalawi poyankhapo za nkhaniyi kuti iye analembera kalata mabungwe osiyanasiyana akufuna kwabwino kuti athandize bungwe lake ndipo anati bungwe la NAC ndi limodzi lomwe lidawonetsa chidwi pothandiza bungweli.
Padakali pano mabungwewa ati alembera kalata mabungwewa komanso mayiko amene amathandiza dziko lino pa chuma, kuti nawo afufuze bwino za nkhaniyi.
Pempholi ladza pomwe mabungwe ena omenyelera ufulu wa anthu maka achinyamata, atapereka masiku khumi ndi anayi ku mabungwe atatuwa kuti akhale atabweza ndalamazi.