Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Francisco Wati Mchitidwe Wozembetsa Anthu ndi Ukapolo Wamakono

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati mchitidwe wozembetsa anthu ndi ukapolo wamakono womwe anthu akukumana nawo.

Papa Francisco wanena izi lachiwiri kulikulu la mpingo wa Katolika ku Vatican pamene atsogoleri a mipingo yosiyanasiyana, amasayinira pangano lolimbana ndi mchitidwewu womwe wakula kwambiri padziko lonse.

Pamwambowo panafikanso mtsogoleri wampingo wa Anglican padziko lonse Archbishop wa ku Canterbury  Justin Welby, atsogoleri a chipembedzo chachisilamu ndi mipingo ina komanso asungwana awiri wa ku Ghana ndi wa ku Mexico omwe adapulumutsidwapo kumchitidwewu.

Ngakhale chiwerengero chenicheni cha anthu omwe akhudzidwa ndi mchitidwewu sichikudziwika, malipoti ati anthu pafupifupi 35 miliyoni ndi omwe akhudzidwa ndi mchitidwewu padziko lonse.

Ganizo losayinira panganoli linadza mchaka cha 2013, Papa Francisco atakumana ndi mtsogoleri wampingo wa Anglican atazindikira kuti mchitidwe wozembetsa anthu wakhudzanso kwambiri mipingo iwiriyi.

Komiti yoyendetsa ntchito zolimbana ndi mchitidwewu la Globe Freedom Network, linakhazikitsidwa pambuyo pa mkumano wa atsogoleri awiriwa kuti liziphunzitsa anthu za kuyipa kwa mchitidwewu womwe mipingoyi ikufuna kuti uthe pomafika mchaka cha 2020.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>