Unduna wofalitsa nkhani lachinayi wapereka zotsatira za kafukufuku yemwe amachitika kunyumba ya boma pankhani ya kubedwa kwa ndalama za boma.
Kafukufukuyu wasonyeza kuti mtsogoleri wakale wa dziko lino Mayi Joyce Banda wakhala akukumana ndi a Oswald Lutepo womwe adayamba kale kuyimbidwa mlandu pankhaniyi.
Zithunzi zomwe makamera akunyumba ya bomayo adajambula, akuti zasonyeza kuti mtsogoleri wakaleyu adakumanapo ndi a Lutepo komanso nduna zina za boma maulendo 23 kunyumbayo, nkhani yakubedwa kwandalamayi isadadziwike.
A Lutepo adawuza wayilesi ina mmbuyomu kuti amkachita kutumidwa ndi mtsogoleri wakale wa dziko linoyu kuti akabe ndalamazo.
Iwo apempha boma kuti lipereke kanema zomwe zinkajambulidwa ku nyumba za boma ya Mzuzu, Kamuzu Palace, Sanjika komanso Chikoko Bay kuti iwonetse zonse zomwe amakambirana ndi Mayi Banda kamba koti zikhonza kukhala mboni.
Pakadali pano undunawu wati wasiya zonse mmanja mwa bungwe lolimbana ndi ziphuphu la Anti-corruption Bureau ACB kuti lifufuze bwino.