Mabungwe anayi owona za ufulu wa achinyamata omwe akugwilira ntchito zawo mchigawo chakumpoto, awopseza kuti achita ziwonetsero ngati mabungwe omwe adatenga ndalama kubungwe la NAC mosavomerezeka, akhale asadabweze ndalamazi pakatha masiku khumi ndi anayi.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi mmalo mwa mabungwewa,mkulu wa bungwe la Youth and Society mu mzinda wa Mzuzu a Charles Kajoloweka ati pakadali pano, mabungwewa akudikira ndi chidwi kuti bungwe la Mulhako wa Alhomwe,bungwe la BEAM Trust lomwe limatsogoleredwa ndi mkazi wamtsogoleri wadziko lino Mai Getrude Mutharika, komanso nthambi yaboma ya ukazitape ,ikhale itabweza ndalamazi pomafika la Mulungu pa 14 mwezi uno.
A Kajoloweka ati padakali pano mabungwewa ayamba kale kukonzekera zomwe adzachite ngati ndalamazi sizibwezedwa.
Iwo ati ndalama zomwe zinatengedwazo kuti zigwire ntchito moyenera kumbali ya matenda a Edzi zingathandize kwambiri maka kwa achinyamata.
“Ife tikutsimikiza kuti tiwonetsetsa kuti ndalamazi zabwezedwa kamba koti ndalamazi si za anthu andale kapena anthu amene akugwira ntchito ndi chipani cholamula,” anatero a Kajoloweka.
Mabungwewa anena izi pomwenso mabungwe a CHRR,CEDEP,MANELERA+MANET+ ndi MEHEN aperekanso masiku asanu ndi awiri kuti mabungwewa abweze ndalamazi ndipo ati ngati sizitheka achitanso ziwonetsero.