Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mugabe Wachenjeza kuti Achotsa Ntchito omwe Akumukonzera Chiwembu

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la Zimbabwe Robert Gabriel Mugabe wachenjeza kuti achotsa ntchito komanso kulanga aliyense yemwe angadziwike kuti akukonza zomuchitira chiwembu.

Pulezidenti Mugabe wanena izi lachinai pamsonkhano waukulu wachipani chake cha ZANU-PF omwenso ukuyembekezeka kumusankha kuti apitilize kukhala mtsogoleri wachipanichi.

Malipoti ati wachiwiri kwa Pulezidenti wadzikolo Mai Joyce Mujuru, omwenso akuganiziridwa kuti ndi mmodzi mwa anthu omwe amakonzera  a Mugabe chiwembu, sadali nawo pa msonkhanonowo pamene pulezidenti Mugabe amalankhula izi.

Pulezidenti Mugabe,yemwe pano ali ndi zaka 90 zakubadwa, wakhala akulamulira dziko la Zimbabwe kuyambira mchaka cha 1980 pomwe dzikolo lidapeza ufulu odzilamulira.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>