Atsikana amene anasiyira sukulu panjira kamba ka zifukwa zosiyanasiyana akuti ali ndi mwayi wotha kukapitiliza maphunziro awo ndi thandizo lochokera ku bungwe lomwe angolikhadzikitsa kumene la Foundation for Civic Education and Social Empowerment.
Mkulu wa bungweli Mayi Mirriam Chilemba ndi amene anena izi pomwe amafotokozera mtundu wa a Malawi zambiri za bungweli m’boma la Balaka.
Mayi Chilemba ati aganiza zokhadzikitsa bungweli limodzi ndi anthu a m’bomalo pofuna kuthandiza kukweza maphunziro a atsikana ndinso kuthandiza anthu olumala powapatsa upangiri wabwino wothandiza pachitukuko cha miyoyo yawo.
“Tizipereka zoyenera monga uniform ndi zina zofunika za kusukulu kuti asamapezenso mavuto ena amene amakumana nawo komanso tinagula makina osokera a anthu olumala kuti azichita bizinesi,” anatero Mayi Chilemba.
Bungweli liyamba kugwira ntchito zake m’madera a mafumu akulu Sawali ndi Mkaya m’boma lomwelo la Balaka.