Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la Chilungamo ndi Mtendere CCJP Silikukhutira ndi Kayendetsedwe ka Ntchito za Boma.

$
0
0

Bungwe la Chilungamo ndi Mtendere CCJP mu mpingo wakatolika lati silokhutira ndi momwe boma likuyendetsera ntchito zake pofuna kutukula miyoyo ya anthu mdziko muno.

Bungweli lanena izi kudzera mchikalata chomwe latulutsa pambuyo pamsonkhano wa akuluakulu wa bungweli ochokera mmadayosizi onse wowunika momwe zinthu zikuyendera mdziko muno pambuyo pachisankho cha patatu.

Chikalatacho chati kawuniwuni wa bungweli wasonyeza kuti mmiyezi isanu ndi umodzi yapitayi dziko lino litasankha atsogoleri atsopano, tsogolo lenileni la a Malawi silikuwoneka bwino.

Bungweli lapempha boma kuti liziyendetsa zinthu zake ndi masomphenya,  maka pa ntchito yotukula dziko lino kamba koti pali zinthu zochepa zomwe dziko lino lingaloze kuti likuchita bwino monga kukhala moyo wa bata ndi mtendere, kukhwima maganizo kwa anthu podzudzula zinthu zimene zikulakwika mdziko muno komanso kulimbikira ntchito kwa amalawi pofuna kudzipezera thandizo pakati pa mavuto amene akukumana nawo.

Chikalatacho chatinso bungwe lolimbana ndi katangale la Anti Corruption Bureau ndi losakwanira polimbana ndi mchitidwe wa ziphuphu, ndipo pakufunika kuti boma liyike phunziro la padera lokhudza katangale ndi ziphuphu, pofuna kuti ana azikula akudziwa za kuyipa kwa mchitidwewu.

Bungweli lapempha boma, mabungwe osiyanasiyana ndi onse okhudzidwa kuti kuti achitepo kanthu kuti miyoyo ya anthu isinthike.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>