Mtsogoleri wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wati ndi wokhumudwa kwambiri ndi imfa ya apolisi asanu ndi anayi omwe amwalira loweruka pangozi ya galimoto m’boma la Balaka.
Malinga ndi chikalata chomwe unduna wofalitsa nkhani,zokopa alendo ndi chikhalidwe watulutsa, Pulezidenti Mutharika ndiwokhudzidwa kwambiri ndi imfa ya apolisiwa omwe amwalira m’bomalo paulendo woperekeza Pulezidenti ku mwambo wolonga mfumu yayikulu Kapoloma m’boma la Machinga.
Chikalatacho chati Pulezidenti Mutharika akupepesa kwa mkulu wa apolisi, mabanja ofeledwa, komanso anthu onse, ndipo walonjeza kuti achitapo kanthu kwa mabanja omwe akhudzidwa ndi imfayi panthawi yovutayi.
Galimotolo lachita ngozi, dalayivala wake atalephera kuliwongolera pakona.