Akhristu a mu Parish ya St.Charles Lwanga mu dayosizi ya Zomba awayamikira chifukwa chothandiza Radio Maria Malawi.
Bambo Patrick Mwaliwa amalankhula izi pa mwambo wa misa ya promotion womwe unachitika lamulungu pa 7 December 2014 ku parishiyo.
Iwo alimbikitsa akhristu onse a mparishiyi kuti apitilize kuthandiza wailesiyi mu njira zosiyanasiyana zimene angakwanitse.
“Munthu amene amathandiza Radio Maria amathandiza kufalitsa uthenga wa Ambuye kwa anthu ochuluka mu nthawi yochepa,” anatero Bambo Mwaliwa.
Pa mwambowo anthu anathandiza Radio Maria Malawi ndi ndalama zokwana 4 hundred 31 thousand ndi 7 hundred kwacha komanso katundu osiyanasiyana.
Mwambo ngati womwewu unachitikanso ku tchalitchi la Matawale yomwe ndi nthambi ya St.Charles Lwanga Parish.
Bambo Mcdonald Kankhono womwe ndi Bambo Mfumu a ku St.Charles Lwanga Parish anathokoza komanso kulimbikitsa abwenzi chifukwa cha ntchito yayikulu yomwe iwo akugwira pothandiza kupeza thandizo loyendetsera wailesiyi.
Pa mwambowo panapezeka ndalama zokwana 177 thousand kwacha.