Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kudzidalira kwa Amayi pa Chuma Kungachepetse Nkhaza zomwe Amakumana Nazo

$
0
0

Kudzidalira kwa amayi pa chuma akuti kungathandize kuthetsa nkhanza zochitika pakati pa amayi ndi ana m'dziko muno. 

Mkulu oyendetsa ntchito za bungwe la Centre for Altenatives for Victimised Women andChildren Mayi Joyce Phekani, ndi omwe alankhula izi pa sukulu ya pulayimale ya Malire m'boma la Chiradzulu, pomwe bungwe lawo limakhazikitsa masiku khumi, asanu ndi limodzi othana ndi nkhaza zochitika pakati pa amayi ndi ana.

Mayi Phekani ati nkhaza zambiri zomwe zikuchitika pakati pa amayi ndi ana, zikuchitika kamba koti amayi ambiri, alibe chochita choti mkukwanitsa kukhala moyo wodzidalira akasiyana ndi munthu yemwe akuwachitira nkhanza mbanja.

Pamenepa iwo apempha amayi m'dziko muno kuti alowe mmabungwe obwerekana ndalama m'mudzi kuti adzitha kupeza ndalama zoyambira mabizinezi omwe angathe kuwachititsa kukhala odzidalira. 

Polankhulapo mlendo olemekezeka pa mwambowo Sub T/A Maoni, wati mafumu adzipereka kwathunthu powonetsetsa kuti nkhaza zomwe  amayi ndi ana amachitiridwa zatheratu mdera lake.

Pamenepa mfumuyi yayamikira bungweli kamba kophunzitsa anthu mdera lake zakuyipa kwa mchitidwe wa nkhaza.

 

Mwambo wa masiku 16 olimbana mwapadera ndi nkhanza zam’banja padziko lonse umachitika chaka chilichonse, ndipo chaka chino, mwambowu unayamba pa 25 November, ndipo ukuyembekezeka kutha  pa 11 December.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>