Amayi a mu Parish ya Kausi mu diocese ya Mangochi atsindika kufunika kwa misonkhano ya amayi yomwe ikuchitika mu dioceseyo kamba koti ikuwathandiza kukhala olimbika ndi odzipereka pa chikhristu chawo.
Wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la amayi achikatolika la Catholic Women Organization m’parish-yi Mayi Gloria Masala , ndi amene anena izi pambuyo pa msonkhano wa amayi a bungweli umene umachitikira ku parishiyo.
Iwo ati amayi ambiri mparish ya Kausi atsekuka m’maso ndipo ayamba kudziwa zambiri zothandiza pachitukuko cha mpingo ndi miyoyo yawo ya uzimu kudzera m’maphunziro osiyanasiyana omwe akumalandira.
Mayi Masala ati chitukuko cha mu mpingo chimadzera kwa amayi choncho apempha amayi kuti azitekeseka ndi zochitika zosiyanasiyana za mu mpingo.
“Amayi akuyenera kulowa mmabungwe osiyanasiyana a mu mpingo kuti azitha kuphunzitsana ndi anzawo mmene angayendetsere mpingo,” anatero Mayi Masala.
Ena mwa amayi omwe anali nawo ku msonkhanowu ati apindula kwambiri kamba koti aphunzira zambiri zokhudza chikhristu chawo.
Msonkhanowu unayamba lachisanu pa 5 December ndipo watha lamulungu pa 7 December 2014.