Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

PAPA BENEDIKITO WA CHI 16 ATHOKONZA BUNGWE LA PRO-PETRI-SEDE ASSOCIATION OF BELGIUM

$
0
0

Mtsogoleri wa Mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Benedikito wachi 16, wayamikira bungwe lina la m’dziko la Belgium, chifukwa cha thandizo landalama lomwe limapereka ku likulu la Mpingowu.

Papa Benedikito wachi 16, wapereka kuthokoza kwake pamene  amalankhula kwa mamembala a bungwelo, omwe ali pa ulendo okacheza ku likulu la Mpingowu ku Vatikani m’dziko la Italy.

Papayu  wayamikira mamembala a bungwe, la PRO-PETRI-SEDE ASSOCIATION OF BELGIUM, lomwe limapereka thandizo la ndalama zothandizira  ntchito zosiyanasiyana ku likululo chaka chilichonse, chifukwa  cha chachifundo chawo komanso mtima okonda Mpingo wawo wa Katolika.

 “Akhrisitu, azindikire kuti chikhulupiliro ndi ntchito zachifundo, ndi zinthu ziwiri zomwe zimayendera limodzi ndipo zimadalirana. Chikhulupiro chopanda ntchito zachifundo komanso ntchito zachifundo zopanda chikhulupiliro ndi zopanda tanthauzo”, watero Papa Benedikito wachi 16.

Pokambapo za chaka cha chikhulupiliro komanso nyengo ino ya masautso a Ambuye Yesu Khristu, Mtsogoleri wa Mpingo wa Katolikayu wati nyengo ziwirizi, zikhale mwai waukulu kwa akhrisitu onse mu Mpingowu otembenuka mtima  kuti ayanjanenso ndi Yesu, yemwe satopa kukumana ndi anthu omufunafuna.

“Chaka cha chikhulupiliro komanso nyengo ya masautso a Ambuye Yesu khristu zikhale mwai kwa ife a Katolika kuti titembenuke mtima ndi kuyanjananso ndi Yesu yemwe satopa kukumana ndi anthu omufunafuna", watero Papayu.

Pomaliza, Papa Benedikito wachi 16 yemwe mwa ufulu wake akupuma paudindowu lachinayi pa 28 February chifukwa cha kukula, wafunira mafuno abwino mamembala a bungwelo paulendo wawo okacheza ku likululo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>