Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

DONGOSOLO LA KUTULA PANSI UDINDO KWA APAPA

$
0
0

Mneneli wa Mpingo wa katolika ku VatiKani  Bambo Federico Lombardi apereka dongosolo la momwe zikhalire pomwe mtsogoleri wa Mpingowu akhale akupuma komanso mmene asankhire papa  wina kumapeto a mwezi uno.

Bambo Lombardi ati Papa Benedikito wa 16 adzachititsa msonkhano ndi gulu la ma kadinala pa 28 February 2013 ndipo adzatula pansi udindo wake madzulo ake.

Papayu akadzatula pansi udindo wake akuluakulu a ku Vatikani adzayamba dongosolo ngati lomwe limachitika pomwe Papa wamwalira.

Mtsogoleri wa Mpingo wa katolikayu akuti sadzachita chilichonse chokhudzana ndi dongosolo losankha Papa winayo.

Akuluakulu omwe amagwira ntchito yolangiza  Papa Benedikito wa 16 (Roman Curia) adzatula pansi udindo wawo ndipo akhoza kudzasankhidwanso  potengera Papa amene akudzatenga udindowo.

Ndipo makadinala omwe akhale akusankha Papa watsopano kumapeto a mwezi uno akuti alipo 117 ndipo ambiri mwa iwo ndi achokera m'dziko la Italy.

Makadinala 61 ndi aku Europe, 19 aku Latin America, 14 aku North America, 11 aku asia ndi 11 ena aku Africa. Makadinala 67 ndi omwe anasankhidwa ndi Papa Benedikito wa 16 pomwe 50 anasankhidwa ndi mtsogoleri wakale Papa Yohane Paulo wachiwiri wodala.

Panthawi yosankha Papa wina makadinalawa samaloledwa kuyankhula ndi munthu wina aliyense.

Pakadali pano Bishop Giuseppe Sciacca wasankhidwa mongogwilizira kukhala owona momwe chuma cha ku likulu la Mpingowu ku Vatikani chikugwiritsidwira ntchito.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>