Kumangidwa kwa hostel ya atsikana pa sukulu ya Secondary ya Liwonde m’boma la Machinga kuthandiza kuti atsikana ambiri ayambe kuchita bwino pa maphunziro awo.
Mphunzitsi wa mkulu pa sukuluyi a Welson Magowa ndi amene wanena izi pofotokozera mtolankhani wathu. A Magowa ati atsikana pa sukuluyi akhala akukomana ndi mavuto osiyanasiyana kamba koti akhala akuchokera m’madera akutali ndi sukuluyi, koma zomwe bungwe la WORLD UNIVERSITY SERVICES lachita pothandiza ndi chitukuko cha nyumba yogona atsikana pa sukuliyi zithandiza kwambiri pa ntchito zokweza maphunziro a atsikana m’bomalo.
“Atsikana ambiri amachokera mmadela akutali, ndipo chifukwa chopanda zipangizo zowathandiza pa mayendendwe ngati njinga, zapangitsa atsikana ambiri kutenga pathupi, chifukwa chokhulupirira anthu ena omwe amaoneka ngati akuwathandiza mapeto ake nkuwapatsa mimba.”anatero a Magowa.
Sukulu ya secondary ya Liwonde m’boma la Machinga ndi imodzi mwa sukulu zaboma imene imachita bwino pa zotsatira za mayeso a Boma.