Makolo ena ku nsanje akupitirizabe kuchita miyambo ina yoipa monga kukwatiwitsa ana akadali achichepere komanso kuwagwiritsa ntchito zokhwima zomwe ati zikumakolezera ana ambiri kusiya sukulu. Mkulu wa bungwe la CONCERN WORLDWIDE Mayi Daisy Nyambi ndiwo anena izi ku Nsanje pomwe bungweli likuchita kampeni yomemeza ana aku pulaimale, makolo komanso adindo za kufunika kwa sukulu.
Iwo ati ana akhoza kudzakhala ndi tsogolo lowala ngati makolo komanso adindo awalimbikitsa pamaphunziro komanso kuwateteza ku miyambo yoipa yosiyanasiyana. Mayi Nyambi achenjezanso anthu m`bomalo kuti kuphwanya maufulu a ana ndi mlandu ndipo anapempha anthu omwe achitiridwa nkhaza kuti adzikanena ku polisi ndi cholinga choti anthu opalamulawo adziyimbidwa mlandu. Bunngwe la CONCERN WORLDWIDE likuyembekezeka kufikira masukulu 17 m`bomalo.