Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kupempherera Atumiki Ampingo ndi Udindo wa Akhirisitu

$
0
0

Akhristu ampingo wa katolika ati ali ndi udindo opepherela atumiki a mumpingowu kuti asataye utumuki wawo.

 Episcope wa arkdiyosizi ya Blantyre Ambuye Luke Msusa ndiwo anena  izi  pamwambo wa malumbiro oyamba a asisteri asanu ku likulu la chipani cha asisteri  Sisters of our Lady  ku Stella Maris mu m’dzinda wa Blantyre. Ambuye Msusa anati makolo ambiri lero amayembekezera thandizo la zachuma kwa ana awo omwe ndi atumiki a Mulungu zomwe zikuchititsa atumikiwa kuiwala ntchito yawo yotumikira m`munda wa Ambuye.

“Muzitipempherera ife atumiki anu, ndipo mmene mwatilepereka ku mpingo musaembekezere phindu koma mapemphero athu,chifukwa mukayembekezezera phindu atumiki anu ayiwala utumiki wawo ndipo ayamba ma bizinesi” anatelo Ambuye Msusa

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>