Sukulu ya ana osamva ndi kulankhula ya Chisombezi m’boma la Chiladzulu yapempha anthu m’dziko muno kuti azikonda kulimbikitsa ntchito zopeleka thandizo kwa anthu olumala ndikuti nawo azitha kukhala moyo wosangalala.
M’modzi mwa akuluakulu a sukuluyi Sister Emma Kulombe ndi amene anena izi polankhula ndi Radio Maria . Iwo ati anthu olumana , monga osamva ndi kulankhula amakhala akusowa zambiri pa miyoyo yawo , choncho ndi udindo wa aliyense kuonetsetsa kuti akutengapo mbali pothandiza anthu-wa.
“Mulungu analenga munthu muchifaniziro chake ndipo ndi cholinga chamulungu kuti tonsefe tiwathandize pazosowa zawo,tilowe mmoyo wawo kuti tiwamvetse”anatelo Sister Kulombe,ndipo iwo apempha boma kuti lichite kaundula wa anthu osamva ndi kulankhula kuti ziziwike kuti alipo angati, kuti choncho athe kumathandizidwa mosavuta.
Pamenepa Sister Kulombe ati sukulu yawo ndi yokonzeka kulandira ana amene ali ndi vuto losamva ndi kulankhula kudzaphunzira nawo pa sukuluyi .