Mpingo wa katolika mdziko la Iraq wapempha anthu mdzikolo kuti asale zakudya lisanafike tsiku la khirisimasi, pofuna kupempha chifundo cha Mulungu pakati pa akhristu omwe athawa kuzunzidwa mdzikolo kamba ka chikhulupiliro chawo.
Mkulu wa mpingowu mdzikolo Patriarch Raphael Louis Sako wapempha anthu kuti adzayambe kusala zakudya zawo kuyambira pa 22 mpaka pa 24 mwezi uno,ndipo walangizanso anthuwo kuti achepetse zikondwelero zomwe zimachitika pa 25 December komanso pa 1 Junuary, pofuna kulumikizana ndi akhristu anzawo omwe ali pamavuto.
Iye wati mmalo mwake panthawiyi,akhristu akulimbikitsidwa kusala komanso kuchita ntchito zachifundo maka kwa anthu omwe akukumana ndi mavuto maka kuchigwa cha mapiri a ku Nineveh ndi Monsul ,kuti Mulungu awachitire chifundo pothetsa mavutowo.