Akhristu a mu Parish ya St.Augustine Mangochi Cathedral mu dayosizi ya Mangochi awayamikira chifukwa chothandiza Radio Maria Malawi.
Mkulu woona za chithandizo ku wailesiyi Mayi Veronica Manyozo ndi omwe ayamikira akhristuwa pa mwambo wa nsembe ya misa ya promotion womwe unachitika ku parish yi lamulungu pa 14 December.
Iwo alimbikitsa abwenzi a wayilesiyi komanso akhristu kuti asatope ndi ntchito yayikulu yomwe akugwira pothandiza kupeza thandizo loyendetsera wailesiyi.
Bambo mthandizi wa Parish yi Bambo Fanuwel Masakatila anathokoza akhristuwa kamba ka chidwi chomwe ali nacho chothandiza wailesiyi ndipo awambikitsa kuti apitilize kuyithandiza mu njira zosiyanasiyana zimene angakwanitse.
Pa mwambowu anthu anathandiza Radio Maria Malawi ndi ndalama zopitilira 2 hundred thousand kwacha.