Msonkhano wawukulu wa bungwe la amayi la Catholic Women Organisation (CWO) wayamba dzulo ku sukulu ya sekondale ya asungwana ya Mary Mount mu mzinda wa Mzuzu.
Msonkhanowu unatsekulilidwa lachinayi ndi nsembe ya misa yomwe anatsogolera ndi episkopi wa dayosiziyo Ambuye Joseph Mukasa Zuza,omwenso ndi wapampando wa bungwe la maepiskopi mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi,ECM.
Amayi ochokera mmadayosizi onse a mpingowu mdziko muno ali nawo kumsonkhanowo komwe akukambirana nkhani zosiyanasiyana zokhudza mpingo komanso dziko.
Ambuye Zuza ati,amayi akuyenera kukhala anthu achitsanzo,akuyenera kubweretsa chikondi mbanja, mu mpingo ngakhalenso mdziko ndi cholinga chakuti zonsezi zipite patsogolo.
Wapampando wa bungwe la amayi mdziko muno mayi Bennadeta Chiwaya ati cholinga cha msonkhanowu ndi kumva ma lipoti ochokera mma dayosizi onse ofotokoza mmene bungwe la amayi likuyendera komanso kuphunzitsana ziphunzitso zosiyanasiyana zimene zingatukule mpingo ngakhalenso dziko.
Msonkhanowu womwe mutu wake ndi amayi akatolika wobzala chiyembekezo takupatulani kuti mubereke zipatso ndi wa masiku atatu ndipo ukuyembekezeka kutha pa lamulungu pa21 December.