Anthu oposa makumi atatu aphedwa ndinso ena pafupifupi zana limodzi, abedwa ndi zigawenga mmudzi wina mdziko la Nigeria.
Mmodzi mwa anthu omwe apulumuka pachiwembucho,wawuza wayilesi ya BBC kuti pachiwembucho, achinyamata,ana ndi amayi ndi omwe aphedwa ndi achiwembuwo.
Malipoti ati chiwembuchi chanachitika lamulungu lapitali, koma nkhaniyi yangodziwika kumene anthu omwe apulumuka pa chiwembuchi atafika mu mzinda wa Maiduguri momwe athawira.
Pakadali pano asilikali a mdziko la Cameroon alengeza kuti apha mamembala 116 a mgulu la Boko Haram la mdziko la Nigeria omwe amafuna kuchitira chiwembu malo ena a asilikaliwo.
Palibe gulu la zauchifwamba lomwe lawulula kuti ndi lomwe lachita zichiwembuzo, koma anthu akukaikira zigawenga za Boko Haram kuti ndi zomwe zachita izi.