Bungwe lolimbana ndi matenda a Edzi mdziko muno la National Aids Commission NAC,lakana kulandira ndalama zokwana 5 miliyoni kwacha zomwe anthu ena amalonda anakabweza ku bungwelo mmalo mwa bungwe la mkazi wa mtsogoleri wadziko lino la Beam Trust.
Bungwe la Beam Trust lomwe likufunitsitsa kuti mmizinda ya dziko lino idzikhala yaukhondo, lidalandira ndalamazi ku bungwe la NAC pofuna kuti liyendetsere ntchito zake, koma mabungwe omenyelera ufulu wa anthu atadziwa izi, anagwirizana zokakamiza bungweli kuti libweze ndalamazi pazifukwa zoti ntchito zake sizikukhudzana ndi zolimbana ndi matenda a Edzi, komanso kuti, lidatenga ndalamazi mosavomerezeka.
Anthu khumi omwe akudzitcha kuti amachita malonda mu mzinda wa Lilongwe, anakapereka ndalamazi kwa mabungwe omwe akhala akukakamiza bungwe la Beam Trust kuti libweze ndalamazi kuti akapereke ndalamazi mmalo mwa bungweli, koma bungwe la NAC lakana kuzilandira.