Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu 26 Afa ndi Mabomba M’dziko la Nigeria

$
0
0

Anthu 26 afa mabomba ataphulika mchigawo cha kumpoto kwa dziko la Nigeria.

Mwa anthuwo,anthu makumi awiri,amwalira pa malo ena okwelera basi mtauni ya Gombe ndipo ena asanu ndi mmodzi amwalira ndi mabomba ena omwe aphulika mtawuni ya Bauchi mchigawo chomwecho.

Padakali pano palibe gulu lomwe lawulula kuti ndi lomwe lachita ziwembuzo,koma malipoti a wailesi ya BBC, ati gulu la zigawenga za Boko Haram,zikuvutitsa kwambiri mchigawocho pofuna kukhazikitsa boma la chisilamu mdzikolo.

Malipoti awailesiyi atinso gulu la Boko Haram,latulutsa kanema yomwe akuwonetsa mamembala a gululi,  akupha anthu pasukulu ina, koma sakuwonetsa komwe chiwembucho chimachitikira.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>