Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Zigawenga Zipha Anthu Oposa Makumi Asanu ndi Limodzi Mdziko la India

$
0
0

 Anthu oposera makumi asanu ndi limodzi afa pakumenyana komwe kwakhala kukuchitika pakati pa mitundu ina m’dziko la India.

Nkulu wa apolisi a dzikoli wauza atolankhani m’dzikomo kuti limodzi mwa magulu omwe amamenyana nkhondowo  ndilochokera m’dera la Bodo, ndipo lakhalanso likulimbana kwambiri ndi apolisi a m’dzikomo kamba koti masiku apitawa apolisiwo akuti anakalanda zida za gululi.

Malipoti ati gulu la zigawenga la mtundu wa Bodo lankhala likulimbana ndi anthu a mdera la Assam lomwe lili ndi chiwerengero chokwera cha anthu otsatira chipembezo cha chisilamu , koma chiwembu cha lachiwiri amalimbana ndi anthu  omwe mtunduwawo si a Assame.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>