Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Atatu Afa Phanga Litawagumukila Ku Salima

$
0
0

Anthu atatu afa phanga lomwe amakumbamo miyala ya mtengo wapatali ya Garnet litawagumukira  m’boma la Salima.

Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergeant Gift Chitowe wati izi zachitika lachinayi pa 25 December m’mudzi mwa Sadzu m’bomalo. Mwa anthu omwe amwalira pangoziyi ndi a Adams Mwale azaka 24 zakubadwa komanso  a  Juston Bajesi azaka 25 zakubadwa ndi mwana wa zaka ziwiri. A Adams Mwale amkachokera m’mudzi wa Mpaliro kwa mfumu yaikulu Chatoloma m’boma la Kasungu ndipo  a Juston Bajesi anali a m’mudzi mwa Sangwa m’dera la mfumu yaikulu Khombedza m’boma lomwelo la Salima.

Miyalayo akuti yakhala ikupezeka m’bali mwa mtsinje wa Lilongwe kuyambira mwezi wa November chaka chino, ndipo anthu mazanamazana akhala akufika kumalowo kukakumba miyalayi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>