Akhristu pafupifupi 100 sauzande anasonkhana kunja kwa tchalitchi la likulu la St Peters Square pofuna kuona komanso kutsanzikana ndi Papa Benedicto wa 16 yemwe akhale akutula pansi udindo wake kumapeto a mwezi uno.
Akhristuwo akuti amaonetsa chikondi chawo kwa mtsogoleri wa Mpingowu pomwe amayankhula mokweza mawu kuti amusowa Papayo.
M’mawu ake Papa Benedicto wa 16 anathokoza aKhristuwo kaamba kopitiliza kumupemphelera pa udindo wake.
Ndipo Kadinala wina wa ku New York m’dziko la America watsutsa malipoti oti iye ndi
yemwe akhoza kusankhidwa kukhala mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse pomwe Papa Benedicto wa 16 akhale akutula pansi udindo wake kumapeto a mwezi uno.
Kadinala Timothy Dolana amalankhula izi pa mwambo wa nsembe ya Misa ku St Partick's Cathedral m’dzikolo.
Kadinala Dolan watsutsa zomwe anthu ena akuganiza kuti iye akhoza kusankhidwa kukhala mtsogoleri wa mpingowu ochokera m’dziko la America koyamba .