Akhristu zikwizikwi anakhamukira ku likulu la Mpingo wakatolika ku Vatikani kukalandira madalitso ochokera kwa mtsogoleri wa Mpingowu pa dziko lonse Papa Benedikito wachi 16 pa umodzi mwa miyambo yake yotsiriza ali pa udindowu.
Polankhula kwa akhristu omwe anasonkhana pa bwalo la likulu la St Peters Square, Papa Benedikito wachi 16 wathokoza anthu onse omwe akhala akumupempherera komanso kukhala naye limodzi kuchokera pomwe analengeza zakutula pansi udindo wake kumapeto kwa mwezi uno.
“Ndikuthokoza anthu nonse amene mwakhala mukundipempherea komanso kukhala nane limodzi kuchokera pomwe ndinalengeza za kutula pansi udindo wanga ku mapeto a mwezi uno”, watero Papa Benedikito wa chi 16.
Papa wapemphanso akhristu kuti akhale obadwa mwatsopano pachikhulupiriro chawo mwa Mulungu.
“Ntchitoyi ndi yayikulu kwambiri ndipo akhristu tikuyenera kuigwira ngati asilikali omwe akumenya nkhondo”, watero mtsogoleri wa Mpingo wa Katolikayu.