Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Makhansala Apempha Boma kuti Liwapatse Ngongole

$
0
0

Bungwe la makhansala mdziko muno la Malawi Local Government Association (MALGA), lapempha boma kuti lipereke ngongole yogulira njinga za moto yomwe lidalonjeza kuti lipereka kwa makhansala  pofuna kuti ntchito yawo iziyenda bwino.

Pulezidenti wa bungweli a Samson Chazeya, anena izi pomwe mtolankhani wathu amafuna kudziwa kuchokera ku bungwe lawo,zina mwa zifukwa zomwe zikulepheretsa makhansala kugwira bwino ntchito zosiyanasiyana mmadela awo chiponyere voti pa  20 May chaka chatha.

Iwo ati vuto la mayendedwe, ndi limodzi mwa mavuto omwe boma likuyenera kukonza, pofuna kuti ntchito za makhansalawa ziwonekere poyera.

A Chazeya ati kusagwirizana kwa pakati kwa iwo ndi aphungu a ku nyumba ya malamulo makamaka pa uthenga mmene angagwilire ntchito zawo ndi zina zimene zikupangitsa kuti ntchito za makhansala zisamawoneke.

Padakali pano makhansalawa akuyembekeza kuti boma lichitepo kanthu pa pempho la ngongole yogulira njingazo


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>