Zokonzekera mwambo otsekulira chikondwelero chakuti sukulu yosulira ansembe ya Kachebere m’boma la Mchinji yatha zaka 75 chiyambire ntchito zake akuti zikuyenda bwino.
Wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa ntchito zokonzekera chikondwelerochi Bambo George Nyanga ndi omwe anena izi lachitatu polankhula ndi Radio Maria Malawi.
Bambo Nyanga ati mwambo otsekulira chikondwelerochi, uchitika loweruka pa 10 mwezi uno,ndipo pa 10 October 2015 ndipamene chikondwelerochi chizachitike.
Iwo ati zokonzekera za chikondwelerochi zikuyenda bwino kamba koti akhazikitsa ma komiti osiyanasiyana omwe akugwira ntchito yokonzekera mwambowu.
Mwambo otsekulira chikondwelerochi loweruka likudzali, udzayamba ndi nsembe ya misa yomwe ikuyembekezeka kudzatsogoleredwa ndi Episkopi wa Dayosizi ya Karonga Ambuye Martin Mtumbuka,omwenso ndi wapampando oyang’anira ntchito msukulu zosulira ansembe mdziko muno.