M’tsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati ndi wokhudzidwa ndi imfa ya atolankhani a ku kampani ina yolemba nkhani omwe aphedwa lachitatu mu mzinda wa Paris m’dziko la France.
Mu uthenga omwe likulu lampingowu ku Vatican latulutsa, Papa wati imfa ya anthuwa, omwe anachita kuwombeledwa ndi anthu ena osadziwika ,yasokoneza mtendere m’dziko la France .
Padakalipano apolisi mdzikolo akuti agwira anthu asanu ndi awiri powaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya atolankhaniwo.