Bungwe la Rights Advice Center m’boma la Mangochi lati lakonza mapulani omwe athandize kuthana ndi m’chitidwe wozembetsa anthu m’bomalo.
Mkulu wa bungweli m’bomalo a Madalitso Masache ndi yemwe wanena izi pofotokozera mtolankhani wathu , yemwe amafuna kudziwa ntchito zomwe bungweli lakonza kuti ligwire m’chakachi.
Iwo ati bungwe lawo litachita kafukufuku, lapeza kuti mchitidwe wozembetsa anthu ukupitilira m’boma la Mangochi.
“Tagwirizana ndi bungwe la Ma Judge komanso ma Magistrate kuti asule anzathu apolisi komanso a Immigration maka amene amakhala malire adziko pa nkhani zozembetsa anthu, komanso tikhala ndi maphunziro mmadera osiyanasiya owaziwitsa anthu kuyipa kwa mtchitidwe ozembetsa anthu”, anatero a Masache.