Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Makwaya a Amayi Awalimbikitsa kuti Apitilize Kudzipereka mu Mpingo

$
0
0

Mamembala a makwaya a amayi mu mpingo wakatolika mu dinale ya Thyolo awalimbikitsa kuti apitirize kudzipereka pogwira ntchito zotumikira Mulungu kudzera mu mphatso ya mayimbidwe.

Mlembi wa mu komiti ya ma kwaya mu dinaleyi Mayi Regina Lambati ndi womwe anena izi pa kwaya festival ya makwaya a amayi mu dinaleyi.

Iwo ati komiti yawo ndi yokondwa ndi momwe amayi akudziperekera pa ntchito zofalitsa Uthenga wabwino kudzera mu kuyimba nyimbo za uzimu, zomwe ati zikusonyezeratu poyera kuti amayiwa ayamba kudziwa za udindo umene ali nawo pogwira ntchito zotumikira mpingo.

Pamenepa Mayi Lambati apempha amayiwa kuti asafooke koma kuti apitirize kutumikira Mulungu kudzera m`mayimbidwe.

Makwaya amayi oposera makumi atatu (30)ochokera m`maparish a Bvumbwe, Thunga, January, Thyolo ndi Mitengo ndi omwe anatenga nawo mbali pa festival-yi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko