Ansembe komanso Asemino m`dziko muno awalimbikitsa kuti azipemphera mosalekeza kuti akhristu athe kupulumutsidwa.
Mkulu woyang`anira ma seminale mu mpingo wa Katolika Ambuye Martin Mtumbuka ndi womwe alankhula izi pa mwambo wa nsembe ya misa yotsekulira zochitikachitika za chikondwelero choti Seminale ya Kachebere yakwanitsa zaka 75 chiyikhazikitsire.
Ambuye Mtumbuka womwenso ndi Episkopi wa dayosizi ya Karonga anati pemphero ndi chida chomwe chimamanga unsembe.
Iwo anatsindika kuti palibe chifukwa choti munthu akhale wansembe ngati sakonda kupemphera ndipo akuyenera kuvomereza kuti kusankhidwa kwawo ndi chiyitanidwe.
Pamenepa iwo apempha anthu akufuna kwabwino kuti atengepo gawo pothandiza sukuluyi kamba koti asemino ophunzira pa sukuluyi amakhala ochokera mmadayosizi ozungulira dziko lino.
Mwambo wokondwerera chikondwerero chakuti seminale yatha zaka 75 chiyambire udzachitika pa 15 October 2015.