Nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi yati boma la Chikwawa ndi lomwe lakhudzidwa kwambiri ndi ngozi ya madzi poyerekeza ndi maboma ena pamene mvula yamphamvu ikugwa mmadera ambiri mdziko muno.
Mkulu wowona ntchito za munthambiyi a James Chiusiwa,ndi yemwe wanena izi Lamulungu pomwe nthambiyi, imapereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu omwe nyumba zawo zagwa ndi madzi osefukira mmadera a Makawa komanso Namkumba m’boma la Mangochi.
A Chiusiwa ati mabanja oposa mazana asanu ndi limodzi 600, ndi omwe akhudzidwa ndi ngoziyi pakadali pano m’boma la Chikwawa, ndipo ku Mangochi,mabanja oposa 450 ndi omwe akhudzidwa.
Bungweli lati pamene layamba kupereka thandizo kwa anthu omwe akhudzidwa mmaboma osiyanasiyana, likukonzanso zochita kawuniwuni yemwe athandize kudziwitsa anthu malo oyenera kumangapo nyumba komanso oyenera kugwiritsidwa ntchito zina maka mmaboma omwe amakhudzidwa kwambiri ndi ngozizi,pofuna kupewa ngozi za mtunduwu mtsogolo.
Polankhulapo phungu wa dera lapakati m’boma la Mangochi a Clement Chiwaya, wayamikira boma chifukwa chopereka thandizo mwachangu kwa anthuwo omwe akuti analibe chilichonse chowathandiza pamoyo wawo pambuyo pangoziyi.