Gulu la za uchifwamba la Al Qaeda mchigawo chakumpoto kwa Africa, lawopseza dziko la France ndi ziwembu, pambuyo pa za mtopola zomwe anthu ena, achita mdzikolo sabata yapitayi.
Malinga ndi chikalata chomwe gululo latulutsa pa makina a internet, chati dziko la France likumana ndi zamtopola zosiyanasiyana chifukwa cha nkhanza zomwe dzikolo lakhala likuchita mmayiko achisilamu posawerengera kuti mayikowa ndi oyima pawokha.
Chikalatacho chapitilira kunena kuti ngati asilikali a dziko la France apitilize kukhala mmayiko ngati a Mali ndi Central Africa, komanso ngati nyumba zowulutsa mawu mdzikolo sizisiya kunyoza Mneneri Muhammed, dzikolo liyembekeze zoyipa zambiri.
Anthu anawombera ndi kupha anthu khumi ndi awiri pa kampani ina yotsindikiza nkhani asanachite chiwembu china pa sitolo yina mdzikolo pomwe anaphanso anthu ena.