Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha magulu osiyanasiyana kuti azilemekeza ufulu wa anthu komanso kuwonetsa umodzi pa zochitika zawo.
Papa Francisco wanena izi mdziko la Sri Lanka pamene amayamba ulendo wake wamasiku asanu ndi limodzi woyendera mayiko a ku Asia.
Mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu akuyembekezeka kukafikanso mdziko la Philippines, ndipo pali chikonzero choti m`maiko omwe ayendere,azitsogolera mwambo wa misa m`mabwalo omwe anthu amasonkhana pazochitika zawo zosiyanasiyana.
Ulendowu ndi woyamba Papa kuyendera akhristu aku Sri Lanka chithereni nkhondo yapachiweniweni pafupifupi zaka makumi anayi zapitazo.
Mtsogoleri watsopano wa dzikolo walonjeza kuti athetsa nkhanza zomwe zipembedzo zing’onozing’ono mdzikolo zimachitiridwa.
Polankhula atafika pa bwalo la ndege la Colombo, Papa Francisco anati mtendere ungapezeke polimbikitsa zinthu zimene zimabweretsa umodzi, kugwirizana komanso kuthetsa kusakondera.
Iye anatinso kutsata chilungamo ndi kofunika maka polimbikitsa umodzi.