Ziwonetsero zofuna kukakamiza mabungwe omwe analandira thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe lowona za matenda a Edzi mdziko muno la National Aids Commission NAC kuti abweze ndalamazi zachitika lachiwiri mmizinda yonse mdziko muno.
Paziwonetserozi mabungwe omenyerera Ufulu wa anthu mdziko muno,apereka chikalata chamadandaulo awo pa nkhaniyi.
Kudzera mchikalatachi,mabungwewa awopseza kuti ngati mabungwe omwe analandira thandizoli kuchokera kubungwe la NAC sabweza ndalamazi pasanathe masiku 100, achita zinthu zomwe chikalatacho sichidanene.