Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco, wafika mdziko la Phillipines paulendo wake wa masiku asanu ndi limodzi oyendera mayiko aku Asia. Pakadali pano akhristu a mpingowu ndi ena akupitiliza kufika mu mzinda wa Manila komwe Papa atsogolere zochitika zosiyanasiyana. Polankhula pa mapemphero a mthenga wa m’njelo kwa mai Maria dzulo mdziko la Sri-Lanka,Papa Francisco wapempha anthu mdzikolo kuti ayanjane maka mitundu yomwe yakhala ili pankhondo. Iye wati mtima okhululuka,umayambira pomwe munthu wayamba wavomereza kulakwa kwake pachinthu chilichochonse chomwe chadzetsa kusamvana. Iye walangiza anthuwo kuti atengere moyo okhululuka ngati wa mai Maria,omwe adawonetsa pokhululukira anthu omwe adapha mwana wawo Yesu Khristu pomupachika pa mtanda.
↧