Bungwe la ma Episkopi a mpingo wa katolika mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM) likudziwitsa za imfa ya Olemekezeka Ambuye Joseph Mukasa Zuza amene anali Episkopi wa dayosizi ya Mzuzu komanso wapampando wa bungwe la ma Episkopi a katolika m’Malawi (ECM).
Malinga ndi uthenga umene talandira, Ambuye Zuza anachita ngozi ya galimoto ndipo amwalira pamene anali kulandira chithandizo kuchipatala cha St John ku Mzuzu.
Padakali pano dongosolo la mwambo wa maliro silidadziwike.
Mzimu wa Ambuye Joseph Mukasa Zuza uuse mu mtendere wosatha.