Mwambo oyika m`manda thupi la yemwe anali Episkopi wa dayosizi ya Mzuzu Ambuye Joseph Mukasa Zuza,uchitika lolemba pa 19 January,2015 nthawi ya 10 koloko m`mawa ku St Peters Cathedral mu dayosiziyo.
Ambuye Zuza,omwenso anali wapampando wa bungwe la ma Episkopi mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM) amwalira lachinayi ku chipatala cha St.Johns mu mzinda wa Mzuzu.
Iwo amwalira galimoto lomwe anakwera litachita ngozi ku Chikangawa.
Malinga ndi dongosolo lomwe bungwe la ma Episkopi la Episcopal Conference of Malawi (ECM), thupi la Ambuye Zuza liyikidwa m’manda ku St.Peters` Cathedral pafupi ndi nyumba ya a Bishop mu dayosozi yomweyo ya Mzuzu ,
Nthumwi ya a Papa mmayiko a Malawi komanso Zambia olemekezeka Ambuye Julio Murat, ndi omwe adzatsogolere mwambo wa misa yotsazikana ndi Ambuyewa.
Ambuye Zuza anabadwa pa 2 October mchaka cha 1955, mmudzi mwa Malembo kwa mfumu yaikulu Mbelwa m’boma la Mzimba.
Iwo anadzosedwa unsembe pa 25 July mchaka cha 1982, ndipo anasankhidwa kukhala episkopi wa dayosizi ya Mzuzu pa 9 March 1995.
Malemu Ambuye Zuza anakhalapo mma udindo osiyanasiyana mu mpingowu mdziko muno komanso ku bungwe la ma Episkopi mdera la ku mvuma kwa Africa la AMECEA.
Ngati wapampando wa bungwe la maepiskopi mdziko muno, Ambuye Zuza amwaliranso ali mkulu wasukulu ya ukachenjede ya Catholic University (CUNIMA).
Mpingo wakatolika mdziko muno udzakumbukira Ambuye Zuza ngati episkopi wachifundo,wamsangala,komanso odzipereka pautumiki wake.