Malipoti ochokera mdziko la Phillipines ati anthu oposa 6 miliyoni ndi omwe adali nawo pa mwambo wa nsembe ya ukalistia yomwe mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco anatsogolera mu mzinda wa Manila Lamulungu lapitali.
Wofalitsa nkhani ku likulu la mpingowu ku Vatican Bambo Federico Lombardi ati aka ndi koyamba kuti anthu ochuluka chotere asonkhane pa mwambo wa nsembe ya ukalistia yotsogoleredwa ndi Papa mu mbiri ya mpingowu.
Mu ulaliki wake Papa Francisco anabwerezanso kutsindika zakufunika kwa banja ku dziko komanso mpingo.
Malinga ndi malipoti uthengawu wakhudza kwambiri anthu m`dzikolo, pamene boma langokhazikitsa kumene malamulo okhudza kulera omwe akulukaulu a mipingo sakugwirizana nawo.
Papa Franciscowati ndi zomvetsa chisoni powona kuti masiku ano, mabanja sakutetezedwa ku zoyipa zosiyanasiyana, zomwe zina mwa izo zikulimbikitsidwa mmapulogalamu a boma kuphatikizapo okhudza kulera.