Bwalo loyamba la Magistrate m’boma la Dowa lalamula mzika 71 zaku Ethiopia kuti zipereke chindapusa cha ndalama zokwana 5 sauzande kwacha aliyense komanso kukakhala ku ndende kwa miyezi itatu, zitapezeka zolakwa pa mulandu wolowa mdziko muno mosavomerezeka.
Anthuwo adagwidwa lachinayi pa 15 mwezi uno, pomwe ankafuna kukalowa ku malo a anthu othawa kwawo a Dzaleka m’bomalo, anthu atatsina khutu apolisi omwe patsikuli anali pantchito yawo yokhwimitsa chitetezo.
Mneneri wa apolisi m’bomalo Sergeant Richard Godfrey Kaponda wauza Radio Maria Malawi kuti anthuwo akamaliza chilango chawo,boma liwatumiza kwawo.
Atawuvomera mulanduwo, wapolisi woyimira boma pa milandu Inspector Ivy Sangwa, anapempha bwalolo kuti lipereke chilango chokhwima kwa anthuwo kamba koti kulowa kwawo mdziko muno kukanatha kudzetsa mavuto ena monga matenda ngati a Ebola, chifukwa cholowa mosatsatira ndondomeko.