Malipoti ochokera mdziko la Niger ati anthu khumi aphedwa, ndipo maparishi ochuluka komanso nyumba za ansembe ndi asisiteri, zatenthedwa mdziko la Niger pa chiwembu chomwe anthu omwe sakudziwika achita kumathero a sabata yatha.
Malipotiwo ati mu mzinda wa Niamey womwe ndi likulu la dzikolo, mwambo wa nsembe ya ukaristia anawulepheretsa, maparishi asanu ndi imodzi atatenthedwa pa ziwembuzo.
Pakadali pano, akhristu 285 mu mzindawo, athawira ku malo a asilikali.
Malipoti a boma ati matchalitchi makumi anayi ndi asanu, ndi omwe atenthedwa pa ziwembuzo.
Mdziko la Niger,muli anthu 17.1 miliyoni omwe 80 pa 100 aliwonse, ndi asilamu, ndipo akhristu alipo ochepa kwambiri.
Anthu akuganizira kuti ziwembuzo, zachitika pokwiya ndi chithunzi chonyoza mneneri Muhamad wa chipembedzo chachisilamu, chomwe nyuzipepala ina mdziko la France, inatsindikiza masiku apitawa,zomwe zidachititsa chiwembu china mdzikolo.
Anthu 17, anaphedwa pa chiwembucho.