Amuna awiri afa pomwe amafuna kufukula chitsime chakuphwa m’mudzi mwa Kadula m’dera la mfumu yayikulu Mlonyeni m’boma la Mchinji.
M’neneri wa apolisi m’bomalo Detective Passwell Manase Phiri wati anthu afawo ndi a Yohane Phiri a zaka makumi asanu, omwe kwawo ndi ku Dedza ndi nzawo wina.
Anthu ozungulira pa malowo akuti analetsa amunawo kugwira ntchitoyo, koma iwo akuti anakakamira.
Amuna awiriwa atalowa pa chitsimecho, anthu anadabwa pomva akukuwa modandaula kuti nkatimo mukutentha ndipo anthu a pa mudzipo anayesetsa njira zosiyanasiyana kuti awatulutsemo koma zinakanika ndipo anthuwo anafera momwemo.
Matupi a anthuwo anawatulutsa mchitsimecho lolemba lapitali pogwiritsa ntchito galimoto la kampani ina yokumba zitsime patatha maola awiri.
Zotsatira za kuchipatala zasonyeza kuti awiriwa amwalira kamba kobanika atasowa m’pweya.